Kodi Baibulo linena ciani pa kukhala m’cikondi munthu asanakwatire kapena asanakwatiridwe / kumacita zogonana asanakhale m’banja?

Funso Kodi Baibulo linena ciani pa kukhala m’cikondi munthu asanakwatire kapena asanakwatiridwe / kumacita zogonana asanakhale m’banja? Yankho Mu Baibulo mulibe liu la Cihebri kapena Cihelene (Cigriki) lonena molunjika za kucita za ciwerewere munthu asanakwatire. Baibulo lidzudzula molimba mcitidwe wa cigololo ndi cimo lina liri lonse lokhuza za cimaso-maso. Monga mwa mau apa 1 Akorinto…

Funso

Kodi Baibulo linena ciani pa kukhala m’cikondi munthu asanakwatire kapena asanakwatiridwe / kumacita zogonana asanakhale m’banja?

Yankho

Mu Baibulo mulibe liu la Cihebri kapena Cihelene (Cigriki) lonena molunjika za kucita za ciwerewere munthu asanakwatire. Baibulo lidzudzula molimba mcitidwe wa cigololo ndi cimo lina liri lonse lokhuza za cimaso-maso. Monga mwa mau apa 1 Akorinto 7:2 “inde” ndiyo yankho yomveka bwino: “Koma cifukwa ca madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.” Mu vesi iri, Paulo anena momveka bwino kuti “mankhwala” akuthetsa mcitidwe wa zadama zina ziri zonse ndi kukwatira basi. Coyamba 1 Akorinto 7:2 akunena bwino mofikapo kuti cifukwa anthu alephera kuzigwira okha pa nkhani iyi, ambiri a iwo akucita zadama ndi ciwerewere ndipo pothandiza, ayenera iwo kulowa m’banja. Ndipo iwo akalowa m’banja adzakwaniritsa ndi kukhutitsa pa zones zoyenera anthu okwatirana.

Cifukwa pa 1 Akorinto 7:2 pali mau akunena za kugonana anthu asanalowe m’banja (cigololo, kaya ciwerewere) ndipo mau onsewo adzudzula mcitidwe wotero pakati pa anthu ndi kudzudzula molimba za ciwerewere. Kugonana munthu asanakwatire ndi cimo lokhuzana ndi cimaso-maso. Pali mau ambiri amene anena za ici, kuti kugonana pamene munthu asanakhale m’banja ndi cimo, ndipo mau ena apezeka pa (Macitidwe 15:20; 1 Akorinto 5:1; 6:13, 18; 10:8; 2 Akorinto 12:21; Agalatiya 5:19; Aefeso 5:3; Akolose 3:5; 1 Atesalonika 4:3; Jude 7). Baibulo lifunitsitsa kuti aliyense akhale woziletsa pa gawo iyi ndi kuyembekezera kuti alowe m’banja. Kukhala malo amodzi (kugonana) kumene Mulungu abvomereza ndi kwa iwo okha okhala m’banja, mwamuna ndi mkazi (Ahebri 13:4).

Kawirikawiri timalingalira za gawo la “zokondweretsa” tikamaona pa gawo la nkhani ya kugwa m’cikondi, mopanga kuganiziranso za gawo lina la kuculukitsana – kubalana. Kukhala m’cikondi pa banja ndi cinthu cokondweretsa, ndipo Mulungu anacilenga kuti zinthu zizikhala tero. Mulungu afuna kuti amuna ndi akazi omwe ali m’banja akondwere ndi zogona pamodzi monga momwe cikwati ciyenera kukhalira. Mu Nyimbo ya Solomoni ndi ndime zina zopezeka Baibulo (monga pa Miyambo 5:19) anena momveka bwino za cikondi cimeneci coyenera m’banja. Koma awiriwo, mwamuna ndi mkazi, ayenera kumvetsa kuti colinga ca Mulungu ndi kuti iwo aculukitsane, akhale ndi zipatso za m’banja. Ndiye anthu awiri akayamba zogonana asanakwatirane kumeneko ndiko kulakwa kwambiri – iwo akulowa m’cikondwerero cymene siciwayenera iwo ngakhale pang’ono ponse, komanso potero atha kupanga munthu kubwalo kwa banja pamene Mulungu Anaika kuti mwana aliyense ayenera kukhala mkati mwa banja.

Apapa sanena molunjika kuti kutero ndi kulakwa kapena ai, ngati mau a mu Baibulo okhuzana ndi kukhala m’cikondi munthu asanakwatire, mauwo akadalondoledwa, matenda opatsirana sakadakhala oculuka tere, kutaya mamimba kukadacepa, ongolowa m’banja popeza zacitika akadacepekeranso, asembe anthu okhala ndi mamimba osafuna ndiocepekeranso, komanso ana ongokula kopanda makolo akadacepekera. Kuzikana, ndiwo mau okha amene Mulungu afuna kuti tiwagwiritse nchito pa gawo iri – tiyembekezere nthawi ya cikwati. Kuzikana kusunga moyo, kusunganso ana, kumapereka ulemu waukulu pakati pa munthu wozisamala, komanso, pamwamba pa zones kumapereka ulemu kwa Mulungu.

[English]



[Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa]

Kodi Baibulo linena ciani pa kukhala m’cikondi munthu asanakwatire kapena asanakwatiridwe / kumacita zogonana asanakhale m’banja?

Similar Posts

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.